Abale ana athuwa tikamakhala nao chonde tiziwaphunzitsa akhale - TopicsExpress



          

Abale ana athuwa tikamakhala nao chonde tiziwaphunzitsa akhale akhalidwe makamakanso akabwera alendo, lero monga tsiku la Eid kunyumba kwanga kunafika alendo chakumasanaku. Ine monga mwini nyumba ndinakagula nkhuku ya lokolo kuti alendo anga asiyanitse ndi nkhuku za mu discount. Nao madam sanachitile mwina kuikazinga mwa luso monga munthu wamai. Zonse zitatheka bwinobwino mpunganso ukununkhira bwino monga tonse timaudziwa mpunga wachimalawi, madam chakudya kukasiya pa sitirum, alendo ndaika chakudya patebulo. Alendotu kuyamba kudya, malingana ndi sound yankhuku alendo sanachitire mwina koma kuswa mafupa mpaka kufika stage yoliza amvekere sweee! sweee! Ndiye mwana kungomva sound imene imatuluka mnyumba wayamba kudabwa, kenako wakasuzumira wapeza anthu aja atapanilira fupa akuliza sweee! sweee! Aaaa guyz mwana wathamanga kukatola mafupa amene anali mu dustbin kukaunjikira alendowo amvekere nane ndilizireniiii! Mwana kukakamira kulephera kumnyengelera ndi yogati kukanika ati ndikufuna alendo nane andilizile fupa, moti alendo angawo achoka ali amanyazi kwambiri. Abale nanga umeneo ndi ulemu?
Posted on: Fri, 09 Aug 2013 17:20:09 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015