Dont shoot me, I just copied from somewhere and I dont even have - TopicsExpress



          

Dont shoot me, I just copied from somewhere and I dont even have the rights to distribute TAKULANDIRANI PANO PA POLY Takulandirani pano pa Poly Mudziwe icho khwalala lotchedwa Masauko Chipembere Adaliyikira m’khundumu mwathumu Omanga msewuwa ankadziwa, ophunzira apa Poly ndi ine dziko Akadandaula osaveka zinthu, azikatseka msewuwo zinthu ziyende msanga Takulandirani Mwafika panomu Ndinu anthu ofunika kwambiri m’dziko la Malawi Mudakapita ku Chanco, enanu bwezi muli a phunzitsi a Tikwere Kapena a sukulu zakwacha Mumvekere, “aphunzitsi, auzeni ana aloze Kalulu ndi Fisi pa bolodi” Apo bi, enanu bwezi mukuphunzira Chichewa Chichewa cheni cheni mpaka zaka zinai Ku sukulu ya ukachenjede timaphunzira mchichewa? Mudakapita ku Bunda Mwafikamu, bwezitu aliyense atamugaira khasu ndi khwangwa Okaswa mphanje ku Dzalanyama Enanu bwezi mukuthena ng’ombe Apo bi, tikucheza panomu, enanu bwezi mukusakaniza manyowa Munthu oganiza ndithu Angapite ku koleji kukaphunzira za manyowa mpaka zaka zisanu? Ku Bundako, M’malo molimbikitsa uchembele wabwino wa anthu Iwotu amalimbikitsa uchembere wa ziweto Mesa m’malimbikira sukulu kukana kulima? Ndichifukwa chake mwadza pano Pathumbi la mitu yokungidwa ndi nzeru zakuya Mudziwe Poly ndiyo imanga Malawi Ku Medicine Nkhope zachimwemwezi bwezi zitatha Masana usiku kuyeza mitembo kokhakokha Nkhope zokongolazi Pano zitakumbika ndi misozi Kusewera ndi zidole mpakana dzuwa tswi Mkalasi ku Mediciniko, Amakhala anthu seven Mphunzitsi akati pangani magulu seven, aliyese amapanga gulu lake Mudakakwanitsa inu? Ku Medicinitu Kulibe kuyambitsa nyimbo mokweza Nanga simaliro samatha Ukatitu wafika pa Medicine Umachita kudziwiratu Uli pasiwa mpaka pamene udzamalize maphunziro ako Ku KCN Anyamata, bwenzi muli ma mid husbands Nanha si atsikana amati ma mid wives Zimatikhudza, akatipeza azathu a ma College akuthengeko Kulephera kuwoloka nseu Ena mpaka kulephera kutuluka Mushoprite, akuti potulukira sapaona Koma mwafika panomu Muphunzira ntchito zosunga Malawi Polytu si College, ndi University Mudzavetsere amati Chancellor College Bunda College Kamuzu College of Nursing College of Medicine Iyi ndi University of Malawi - The Polytechnic Chizindikiro kuti mitsuko yodzadza ndi nzeru zakuya Idachita sung’uza pathundu lino Ku Chanco Bwezi enanu nkhope zitatupa Ndi kachasu wa midzi yaku Chilunga Panotu wokumwa mowa Amamwa mowa wa anthu ophunzira Mwana wa pa Poly Akamayenda ndi anzake Apa Bunda, Chanco, KCN ndi COM Amachita kuwonekera patali Kuti uyo, wapa Poly Mwafika panomu Dziwani tikonda kusewera ndi a Police Ikakhwithima sukulu Timapempha ngati apolice ali pa mpata Komanso ngati chimbaula chili bwinobwino Tithamangitsaneko kulimbitsa thupi Ku KCN Kuli uniform Ku university amavala uniform? Paliponse pamene ayenda Ndi mbe mbe mbe Ku sukulu ya mkaka uniform Ku primary uniform Ku secondary uniform Mpaka ku Universityso uniform? Kwatsala ndiku pisila Tidzangova ayamba kuwapisilitsa ku KCNiko Pano pa Poly Timu ya mpira wamiyendo Ma pulakatisitu imakachitira pa Kamuzu Stadium Pomwe azathuwa amangoimva pa wailesi Mchifukwa chaketu tsono Kholo lizindikira likamalangiza mwana limati “Mwana wanga paja umafuna kukaphunzira kuti?” Mwana akati “ku Chanco” Limamuwuza “Kazisewera mwa ufulu” Opita ku Poly, nthawi yosewera alibe Takulandirani
Posted on: Mon, 17 Jun 2013 11:48:08 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015