FAM SILIDACHOTSE NTCHITO KINNAH PHIRI Zadziwika kuti bungwe la - TopicsExpress



          

FAM SILIDACHOTSE NTCHITO KINNAH PHIRI Zadziwika kuti bungwe la Fam silidachotse ntchito Kinnah Phiri ndi gulu lake. Izi zaululika kuti boma ndilimene lidachotsa ntchito Kinnah ndi gulu lake. Pa mkumano omwe ma affiliate a Fam adachititsa dzulo motsogozedwa ndi Fam, ma affiliate adafuna kudziwa chifukwa chimene Kinnah Phiri adamuchotsera ntchito ndipo Fam silidabise koma kuulura kuti boma kudzera mu unduna wa zamasewero a Enoch Chihana udauza Fam kuti ntchito ya Kinnah Phiri ndi onse omuthandizila yatha. Fam yati idali yodabwa kumva maganizo amenewa kamba kakuti cholinga cha nkuano umene Fam idakumana sudali okachotsa ntchito Kinnah Phiri koma kukangounikira nzeru zoti Malawi ikadachita kuti iyambenso kuchita bwino. Lero, bungwe la Fam likhala likukumana ndipo mwa zina akalengeza za yemwe atenge ream ya Malawi yomwe ilibe Mphuzitsi. Mphekesera zamveka kuti bungwe la Fam likufuna kupelekanso team ya Flames mmanja mwa Kinnah Phiri. Zikachitika kumeneko, tikudziwitsani........@Andy (the undisputed)
Posted on: Sat, 16 Nov 2013 09:03:38 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015