Galaxy Radio Malawi Mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur - TopicsExpress



          

Galaxy Radio Malawi Mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika sabata yapitayi anauza mtundu wa A Malawi kuti pa nthawi yomwe adali mu chitokosi cha polisi ku Lumbadzi mu mzinda wa Lilongwe, pomwe iwo komanso akulu- akulu ena a boma ankawaganizila kuti ankafuna kusokoneza kupeleka kwa udindo kwa Dr Joyce Banda pambuyo pa imfa ya professor Bingu wa Mutharika, kudabwela madotolo ena omwe ankafuna kudzawapima. Mtsogoleri wa dziko linoyu adatinso madotolowo adali atanyamula ma jakisoni omwe adali okayikitsa ndipo zidatengela ena a chipanichi kuwaletsa anthuwa kuchita izi pakati pa usiku. Kutsatira izi malipoti anati mtsogoleri wa dziko linoyu amapenekela ku liwu loti assassination ngakhale kuti iye mwini sadagwiritse ntchito liwuli. Malingana ndi Macmillan English Dictionary, liwu loti assassination litanthauza kuti kupha mwa uchigawenga kapena uchingandanga mtsogoleri wa gulu la anthu kapena mkulu wandale pa zifukwa za ndale. Pakadali pano amene adali nduna yowona za mdziko pa nthawiyo a Uladi Mussa atsutsa kuti boma ndilo lidatumiza madotolowo. Koma kodi cheni cheni nchiti, madzulo ano pa Galaxy FM akulu-akulu a zipani za DPP komanso PP akhala akufotokoza mfundo za atsogoleri awo pa nkhaniyi kuyambira nthawi ya 10 minutes past 6 kufika 5 minutes to 7 madzulo Galaxy FM, The voice of Malawi
Posted on: Thu, 11 Sep 2014 05:58:29 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015