Mulungu si james ayi.Mkulu wina anaganiza zothetsa banja,anaganiza - TopicsExpress



          

Mulungu si james ayi.Mkulu wina anaganiza zothetsa banja,anaganiza mwakuya,nkuluyu anamuuza nkanzi wake:mayi ndikuchoka ndikupita ku nchito ndikatha mwezi umodzi ndiye ndikusiya makiyi awa pa Display akasowa inu mudzachoka pano,mayi anangoti zikomo.Bambo ananyamuka waku nyanja,patatha sabata imodzi anatuma munthu kukaba makiyi aja, ndipo zinathekadi,nkuluyu makiyi atalandila anakondwa kwambiri nawatayila nyanja kuti apite ndi madzi koma Chambo cha njala chinawakha nkumeza,bambo nthawi yobwelera ku nyumba inakwana,kunyumbanso mayi nkhawa zapeza nditani makiyi asowa,mayi anagwada pansi nkupemphera kenako ulendo wa ku msika,anagula Chambo cha flesh atele pochosa matumbo a Nsomba anadabwa makiyi exactly omwe aja,anakangowabwezela pa display,bambo anafika:makiyi anga ndipatseni,mayi anangotenga nkupereka ,bambo pakamwa yasaaa....pempero ndi dilu! inu munapemphera musanagone?, nanga podzuka mwangovumbulukap????.
Posted on: Fri, 09 Jan 2015 21:53:20 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015