1. Boma la ulamuliro wa PP lidanamiza anyamata kuti apita Ku South - TopicsExpress



          

1. Boma la ulamuliro wa PP lidanamiza anyamata kuti apita Ku South Korea kukagwira ntchito 2. Boma la ulamuliro wa PP silikuchitapo kanthu kuteteza Nyanja ya Malawi 3. Boma la ulamuliro wa PP lidaoletsa chimanga Pamene a Malawi ankavutika ndi njala 4. Boma la ulamuliro wa PP lidagwetsa ndalama komabe chuma chinapitilira kusayenda bwino 5. Boma la ulamuliro wa PP limagawa mchenga mmalo mwa feteleza kwa a Malawi 6. Boma la ulamuliro wa PP ndilakatangale ndi ziphuphu zoospa kusiyana ndi DPP/UDF 7. Boma la ulamuliro wa PP lidagula magalimoto amanyado a nduna Pamene zipatala zidalibe mankhwala 8. Boma la ulamuliro wa PP likuononga ndalama ndi maulendo amudziko muno komanso kunja omwe phindu lake silikuoneka kwa a Malawi 9. Boma la ulamuliro wa PP limaononga ndalama zambiri pama alawansi kukagawa ufa wandalama zochepa kwambiri 10. Boma la ulamuliro wa PP limanyoza komanso kutukwana a ndale otsutsa mmalo mokamba mfundo zotukula Malawi 11. Boma la ulamuliro wa PP tidaona maliro akumadulidwa maliseche ku motchale Pamene kuphana ndi umbanda udalinso osasimbika. 12. Boma la ulamuliro wa PP likugwiritsa ntchito nyumba zofalitsa uthenga za radio 1 ndi 2 komanso television ya Malawi molakwika 13. Boma la ulamuliro wa PP likuononga ndalama zomwe zinakakhoza kugula mankhwala muzipatala ndi kubweza ndalama kwa anthu omwe ma kontalakiti awo adathetsedwa mosatsata malamulo 14. Boma la ulamuliro wa PP lidagwilitsa ntchito ndalama mosasamala mubajet ya chaka 2012/2013 ndindalama zopitilira ma billion 15. Boma la ulamuliro wa PP limangomvera zilizonse zomwe azungu akuwauza ngakhale zili zosapindulira a Malawi 16. Boma la ulamuliro wa PP limadana komanso kumenya atolankhani kamba kolemba zinthu zosawakomera 17. Boma la ulamuliro wa PP likumangotseka ma masukulu ndimakoleji kamba kamavuto achuma komanso kudana ndi chilungamo anthu akamadandaula mmene zinthu ziliri mudziko lino 18. Boma la ulamuliro wa PP likuononga ndalama pa milandu yomwe ilibe ntchito komanso yosapindulira a Malawi 19. Boma la ulamuliro wa PP silikuganizila za umoyo wa anthu ogwira ntchito mmboma pankhani ya malipilo komanso ma alawansi awo ngakhale umphawi wafika povuta kwa a Malawi ambiri. 20. Boma la ulamuliro wa PP muzipatala mankhwala ofunikila komanso mafuta agalimoto za ambulansi akumasowa zomwe zikuthandizila kuluza miyoyo ya a Malawi omwe anali ndi udindo otukula dziko lathu lino Zili ndi inu kupitilira kunamizidwa kuti zinthu zili bwino koma ngati muli okonda dziko lanu moganizenso mofatsa. Gawilani anzanu kuti nao awonenso
Posted on: Wed, 19 Jun 2013 12:28:31 +0000

Trending Topics



ademic-Staff-Union-of-Universities-ASUU-on-Monday-began-a-topic-532606656805080">The Academic Staff Union of Universities (ASUU), on Monday began a
Evey: Who are you? V. : Who? Who is but the form following the
Good day today! Put a property up yesterday for sale, sold it

Recently Viewed Topics




© 2015