ADM Chonde ndithandizeni.........Amuna anga anandiyimbira foni - TopicsExpress



          

ADM Chonde ndithandizeni.........Amuna anga anandiyimbira foni atapita ku Theba kuti basi banja yatha ndiyendere yanga chifukwa azibale awo anawauza ndikupanga za uhule.Ndipo anayitanitsa tsikana wina wamudzi mwathu kuno ku Malawi kuti akamukwatire ndikunena pano anamanga banja kumeneko.Akhala naye miyezi isanu ndiye kaya sizikumvana nanenso ndinalimba ntima chifukwa chindisuzulireni patha chaka opanda oro thandizo loti ndiziwagulira chakudya ana omwe ndinabereka nawo. Lero akundiyimbira foni akuti atumiza ndalama ndipangitse passport ndizipita ndi ana kodi pamenepa nditani chifukwa anakwatira nsikana wakuti sindikumudziwa bwino za khalidwe yake komanso kunjako kuli matenda kodi ana anga sindiwasiya pa umasiye ?Nditazikana ndalama zakezo ndilakwitsa zikabwera? Chonde ndithandizeni ndalamatu imaphatu ndipo sizoti ndikuvutika ndikupanga geni ya zobvala ndipo zikuyenda ndinalimba ntima kale inu mukuona bwanji ndifere Joni? ##Linda##
Posted on: Wed, 04 Dec 2013 05:49:30 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015