KODI NDI BALE WANJI? Buleki anakwatira Nalinde. Anabereka ana - TopicsExpress



          

KODI NDI BALE WANJI? Buleki anakwatira Nalinde. Anabereka ana awiri,Giya ndi Befina. Buleki ndi Nalinde atayambana banja linatha ndipo anagawana ana aja motere; mayi Nalinde anatenga Giya, pomwe bambo Buleki anatsala ndi Befina. Then ana aja atakula chomwe chidachitika nchakuti Giya anapereka mimba kwa mai ake a Nalinde ndipo bambo Buleki nawonso anapereka mimba kwa mwana wao Befina. Mbali zonse ziwiri kudabadwa ana. Mwana obadwa pakati pa Giya ndi Nalinde adamutcha Junior. Mwana obadwa pakati pa Buleki ndi Befina adamutcha Msadabwe. QUESTIONS: Maubale alipo osiyanasiyana monga;mchimwene, mchemwali,msuweni,amalume, agogo, muphwa,mdzukulu,etc. Kodi pakati pa Junior ndi Msadabwe pali UBALE?. Ngati UBALE ulipo mungautchule kuti chiyani? Secondly, pakati pa Buleki ndi Befina pali wolakwa ngati alipo ndi ndani? Chimodzimodzi pakati pa Junior ndi Nalinde ngati alipo olakwa ndi ndani? (Amene ayankhe momveka bwino ndimuputitsa ku Brazil kuti akaonere World Cup mwezi wa mawa chifukwa Brazil iseweranso ndi Netherlands mu August, koma ulendo uno akasewerera ku Chipoka pa Kamuzu Stadium ku Portugal. Pano ngakhale continent asintha kudzakhala ku Zambia)
Posted on: Mon, 14 Jul 2014 23:44:30 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015