NEWS: President wa dziko lino professor Peter Mutharika, - TopicsExpress



          

NEWS: President wa dziko lino professor Peter Mutharika, wapempha a Malawi kuti achilimike kupeleka msonkho (tax) pakuti ma donors satipanganso support budget ya dziko lino. Polankhula iye wati tikuyenera kumvetsetsa pakuti ulendo uno dziko la Malawi ligwiritsa ntchito ndalama zathu zomwe, mu ndondomeko yotchedwa zero deficit budget. Izi mtsogoleriyu wayankhula potsatira nkusakondwa kwa aMalawi ena okhudzidwa omwe akudandaula ndi kugwa kwa mphamvu ya kwacha mmasiku ochepa. Pano 1 dollar ikuyima pa K501 malingana ndi ma report a lero zomwe zikuyembekezeka kuti itha kukwera kwambiri pomafika mu december. Mwa zina mmalo ena ogulitsira katundu, wakwera malingana ndi kugwa kwa Kwachaku. Mwachitsanzo Sugar pano mmadera ena akugulitsidwa pa mtengo wa K650 ndipo akuyembekezeka kukwera kwambiri. Nduna ina yaboma yati a Malawi asade nkhawa pakuti ndondomeko ya zero deficit budget sikoyamba kuitsata mdziko muno. Ndondomekoyi idagwiritsidwa ntchito mchaka cha pakati pa 2011-2012 pamene zinthu zinakwera kwambiri kupangitsanso kuti mafuta a galimoto asowe kaamba koti mdziko muno munalibe forex.
Posted on: Thu, 30 Oct 2014 11:40:37 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015