Nthabwalist anatembenuka mtima pano ndi Bornagain. Lero - TopicsExpress



          

Nthabwalist anatembenuka mtima pano ndi Bornagain. Lero Nthabwalist anadzuka mamawa kuyamba kupemphera malilime mkati!....ali mkati mopemphera nthabwalist anayamba kumenya chitseko chaku bafa ndizibakera kuti bam! bam! apa mpaka ana ake Sabina ndi Dipuloma amene anali nkugona pa nthawiyi anadzidzimuka chifukwa cha phokosoli....Nthabwalist anapitilizabe kumenya chitseko chija kwinaku akupemphera nati Yesuuu Yesuuu palibesnso winaa koma ndinu nokha nditsegulireni njira zinthu ziyambe kundiendera...apa nde chitseko chija anayamba kuchimenya kwambiri bam! bam! bam! nditsegulireni mbuye wangaa nditsegulireni... Lero Dipuloma ndi Sabina anapita ku sunday school kenaka aphunzitsi amalankhula nati Yesu amamva ndipo amayankha koma ndisanapitilire alipo apa amene angandiuze kumene Kuli Yesu? Nthawi yomweyo Dipuloma anaimika nkono ine aphunzitsi ine aphunzitsi....amvekere....Yesu amakhala ku bafa lakwathu ndipo zoti amayankha mukunama lero adad amamugogodera pachitseko kuti awatsegulire koma iye ali duu osayankha Good Sunday!
Posted on: Sun, 14 Sep 2014 05:04:56 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015