Nyamata wina anali nawo pampikisano wothamanga, ali - TopicsExpress



          

Nyamata wina anali nawo pampikisano wothamanga, ali chithamangireni anaona kuti kutsogolo kwake kuli anthu awiri. Muntima mwake zinamuwawa ndipo anapemphera kwa mulungu kuti amuonjezere mphamvu kuti mpikisano umenewo apambane nambala one. Ali chipempherereni, chithamangireni nyumba ina kunavumbuluka galu kumuthamangisa kuti amulume, nyamata anathamanga populumusa moyo kwa galu. Anzake omwe anali patsogolo pake aja ataona nzawo akubwera ndi galu anakhota ndikubisala kaye kuti wagalu aduse. Ndipo galu sanamuleke nsanga mpaka pamene anayandikira ground komwe kunali anthu ambiri odikirira number one. Ndipo galu uja anabwerera. Kwaiye anayamika Yehova chifukwa chomuyankha pemphero lake pompopompo. abale anzanga mayankho ena amabweranso ngati chiphinjo kuti iwenso uonese chikhulupiro chako. sinzonse mungapemphe kwa mulungu mungayankhidwe pompo ndipo sinzonse mungapemphezomwe simuzayankhidwa pompo.
Posted on: Fri, 13 Sep 2013 11:47:53 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015