POLITICS Ndale/Judo padzana paja dzuwa likuswa mtengo mwawatukwana - TopicsExpress



          

POLITICS Ndale/Judo padzana paja dzuwa likuswa mtengo mwawatukwana Awo mowathandiza Awa, kuti Awo anyozeke, cholinga Awa awine boma kuti mwina Inunso mugwere mommo. Dzuwa likalowa, kwada, inu kunyumba kwanu mukudya nsima ya nyemba zopanda mafuta zovuwaza basi nkumwera madzi, aja mwawatukwana aja kudya dinner kumwerera wine ndi aja mukuwathandiza aja, ndi kumaseka zawo monga umo adziwira Ndale kuti siudani. Inu mwa umbuli-mbuli nkumazitengera kuntima. Lero aja mumawatukwana aja Awina boma. Aja mumawathandiza aja aluza. Owina ndi Oluza lero alembana ntchito. Inu otukwana ndi kunyoza ozitengera ku mtima aja monga a Yufi ngati Khasu mwalambulira Njira iwo kuti azimwabe Wine Pamene inu basi wapanzera ku Labour Office. iiiiii komadi awa ndima Ufumu Adziko lapansi zoona achabechabe Shaaaaa! #[email protected]
Posted on: Mon, 28 Jul 2014 19:34:36 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015