Read dis carefully Paguza ndi nzake Saguza adakambirana - TopicsExpress



          

Read dis carefully Paguza ndi nzake Saguza adakambirana zopita ku Kamuzu Stadium kt akawonere game ya Bullets ndi MTL Wanderers. Mawa mbanda kucha Paguza adalawira kupita town kukanjiya adamusiya Saguza uja ndipo sadamusazike Saguza atazuka pogona sadamuwonepo Paguza khawa idamugwira mene imakwana nthawi ya nkhomaliro Saguza uja sanadye. Mene imakwana 2:00pm Saguza adaganiza zomusata Paguza uja town,panthawi imeneyi sankaziwa kuti Paguza uja wafikatso ku Stadium kuja atafika mu town ship ya Bangwe mwamwayi adakumana ndi Paguza uja akubwera koma akuyenda pansi.Atafusa za game Paguza uja adayakha zoti game yalephereka chikhalilenicho adasiya anthu akukozeka kuti ayambepo koma iye adabisira zimenezi. Pomwe Saguza uja mwadzulo lake adakumana ndi mbale wake yemwe adamulonjeza kuti akakumane naye ku Stadium kwinaso akapase ndalama zokwana k50,000 koma chifukwa cha boza analuza ndalama. \nde a Malawi anzanga tili ndi vuto lonama ngati sitichepesa tizakhala ngati Paguza/.
Posted on: Sat, 16 Aug 2014 16:10:59 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015