TAWERENGANI KANTHANIKA kuchokera kwa pastor #Joe Panali banja - TopicsExpress



          

TAWERENGANI KANTHANIKA kuchokera kwa pastor #Joe Panali banja lina lake lolemela lomwe limakhala ku France. Bambo wa banja limeneli Mr Victor anali wachuma kwambiri chifukwa anali wamkulu wa company ina yoziwika ku France. Pa nthawi ya tchuthi/ holiday anaganiza zopita kumalo ena kokasangalala ndi banja lake, ali njira galimoto yomwe anakwela inachita ngozi ndipo ana awiri ndi mkazi wake anamwalira pompo. Mr Victor anali wamagazi nthawi zonse akaganiza za imfa ya banja lake. Izi zinachitisa kuti aziganiza kuti Mulungu kulibe ndipo akanakonda akanamwalira. Anayamba kumwa mowa nthawi zonse izi zinapangisa kuwachosa ntchito komanso kuwalanda nyumba yomwe amakhala ya ku ntchito, anasamuka kukakhala kanyumba konyasa malo ena. Azake onse anathawa chifukwa cha umphawi omwe anayamba kuwuona ndpo anakhala kwa nthawi yaitali opanda kucheza ndi munthu. Anaganiza zozipha ndipo anasamba bwino tsiku limenelo ndikuvala suit yooneka bwino. anaganiza zokaziponya pa nyumba zosanjikizana zomwe zinali 50 ndiye atakwela kufika pa numbala 48 anakumana ndi bambo ena omwe anawafunsa kuti akupita kuti ndipo anayankha kuti akupita floor yomaliza nambala. 50. Poziwa kuti nambala 50 munali anthu ophunzira bwino Anawachondelela Mr Victor kuti awalembe ntchito chifukwa wa ntchito wawo yemwe anali mu floor nambala 49 anasiya. Mr Victor anapasidwa zonse zofunika plus nyumba yaikulu. Malo okazipha anasanduka osangalala. Ngati ena mwa inu mukuzuzika ndipo mwaganiza zoipa ndikunenelela kuti zoipa zimenezo zisanduke zabwino mu mwenzi uno wa September.. Ndipo ndikupemphelera kuti mavuto ako asanduke chimwemwe mu week ino.. Zofuna zako zikwanilisidwe Type..Amen! #jean
Posted on: Sun, 01 Sep 2013 06:49:55 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015