#coldblooded Pazikhulupiriro zathu pamakhala matenda - TopicsExpress



          

#coldblooded Pazikhulupiriro zathu pamakhala matenda osiyanasiyana. Mwachitsanzo, Achewa ali ndi nthenda ya tsempho komanso nthomba zimene amati nzosachizika. Pakati pa Alhomwe pali nthenda imene akuti ndi uwithe, yomwenso ilibe mankhwala. Florence Tuwanje wa m’mudzi mwa Tuwanje kwa T/A Chiwalo m’boma la Phalombe adapulumutsapo mwamuna wake kunthendayi. Iye adachitanji kuti apulumutse mwamuna wake? Q. Tangomva za nthenda ya ‘uwithe,’ kodi idayamba liti? A. Inu simuyidziwa? Kwanu nkuti? Chifukwa dzinali timaligwiritsira ntchito ndi ife Alhomwe koma sitidziwa kuti madera ena amati ndi nthenda yanji. Ndi matenda a kalekale ndipo inenso ndidauzidwa ndi agogo anga. Q. Tafotokozani mwina ndiwadziwa…… A. Ndi matenda amene amagwira abambo. Amayi amagwidwanso ndi matendawa koma kusiyana ndi momwe amagwirira abambo. Chimachitika nchakuti thupi limatuluka zidzolo, mwina kutupa kumene. Umafooka, ngakhale m’mawondomu mumafookeratu. Izi zimadziwika ukangodzuka koma si nthawi zonse zotere zingakuchitikire. Q. Malungotu awa? Mumawadziwa malungo inu? A. Achimwene mutanthauza kuti mkulukulune ndisadziwe malungo? Ngati inuyo msinkhu wanuwo mukudziwa malungo ndiye ine ndisawadziwe? Munthu sangandiuze kuti malungo amatani ndipo nditani pamene ndikudwala malungo
Posted on: Sat, 23 Aug 2014 21:42:46 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015