BLANTYRE Episcope wa Arch-diocese ya - TopicsExpress



          

BLANTYRE Episcope wa Arch-diocese ya Blantyre ya mpingo wakatolika, Ambuye Thomas Luke Msusa apempha akhristu mu arkdayosiziyo,kuti adzitekeseka ndi nkhani zachipembedzo kuti miyambo yampingo mu dayosiziyo idziyenda bwino. Ambuye Msusa apereka pempholi loweruka pa 16 AUGUST 2014 , pamwambo okondwelera kuti ansembe atatu omwe ndi BAMBO JOHN CHIMWAZA, BAMBO LAZAROUS ZULANI ndi BAMBO MICHAEL CHIMDELENJI akwanitsa zaka 25 mu unsembe komanso nkhoswe ya arch-diocese-yo yomwe ndi Amai Maria Mfumu kazi ya Mitima yonse. Ambuye Msusa ati akhristu akuyenera kumatekeseka ndi miyamboyi kaamba koti ndi njira yokhayi yomwe ingachititse kuti mpingo upite patsogolo. Iwo ayamikiranso ansembe-wo kaamba kodzipereka pautumiki wawo. Ambuye Msusa apempha maanja kuti alimbike pachikhulupiliro chawo pamene akuti anthu osakhulupilira Mulungu tsopano akufuna kugwiritsa ntchito maanja posokoneza chikhulupiliro mwa Mulungu. Ambuye Msusa akupitiliza kufokoza.
Posted on: Sat, 16 Aug 2014 15:32:32 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015