Dzina langa ndine Tiya kukhalira kuno kwa Phwetekere ku Lilongwe. - TopicsExpress



          

Dzina langa ndine Tiya kukhalira kuno kwa Phwetekere ku Lilongwe. Abale mundithandize ndili ndi mzanga ponda apa ndipondepo timagwirizana zedi, tonse tinalibe abwenzi. Milungu yapitayo panali njonda ina yomwe yakhala ikumufuna mzanga uja koma iye amakana, inayetsa njira zosiyanasiyana mzanga amayikanabe kumufunsa chomwe amayikanila amati samusangalatsa. Ine mwamuna aja anandifunsila pompopompo sindinachedwe ndinavomera nditamuwuza mzanga uja sanaoneke okhumudwa komano chodabwitsa akumapanga zomukopa mwamuna uja, kuntumizira ma uthenga achikondi kumamuwuza kuti mwayi ulipobe zonsezo mwamuna wanga akumandifotokozera, ndinachita kuonanso ma uthenga achikondi mu phone ya mwamuna wanga. Kodi Adm ndimufunse bwanji ameneyu kuti asiye kumvutitsa mwamuna wanga koma ndisaonongotso uchimzake! Ndingapange bwanji?
Posted on: Mon, 09 Sep 2013 02:48:48 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015