Funso (Inbox): Bambo anga adamwalila ndili mwana. Zitatero mai - TopicsExpress



          

Funso (Inbox): Bambo anga adamwalila ndili mwana. Zitatero mai anakwatiwa ndi ena ndipo adandilela mpakana ndinakula ndi kundiphunzitsa mpaka pamene ndilipa. Ine ndinasitha dzinal la bambo ndikumayendera la bambo ondipezawa. Koma nditamva Hadith, ndinasintha nkubweretsanso dzina loyamba lija. Kodi pamenepa ndikazawadziwitsa kuti ndasintha dzina lawo ndipo ndabweretsa la bambo anga, akazavuta ndi zapange chiyani? ---------- Yankho: Zikomo kwambiri chifukwa cha funso iri limene liri lothandiza kwambiri. Choyamba ndiikirepo ndemanga malinga ndi kubwelera kwa dzina lanu; Zimene zakuchitikirani inu brother ndi zomwe zimachitikanso ndi anthu ena osiyanasiyana padziko lapansi, ndipo ndi ochepa amene amaganizira kuti kodi Chisilamu chikuti bwanji pa nkhani imeneyi. Pokhapo Mulungu adzikudalitsani ndikukuonjezerani kuzindikira. Mu kuyankha kwathu pa funso limeneli, tiyeni tione kaye mu QuranYolemekezeka, imene iri nkhokwe ya malamulo oyendetsera Chisilamu komanso umoyo wa munthu wa tsiku nditsiku. Chitsanzo mwachidule kwambiri: Nthawi imene Mtumiki salla Allah alaih wasallam analandira Zaid bun Haarith ngati mphatso kuchokera kwa mkazi wake Khadija radhiaAllah anha nkumamusunga ngati kapolo wake, Zaid anasanduka ngati mwana wa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam, panadutsa kanthawi ndipo dzina lake linasintha kuchoka Zaid bun Haarithah kufika Zaid bun Muhammad. Komatu mmene zimateremu, bambo a Zaid analipo, koma kuti iye sankafuna kukhala nao malingana ndi chikondi chomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kumuwonetsa iye. Patadutsa nthawi, Allah Taala anasitsa Aayah yoletsa zoti ngati mwana akukhala ndi abambo ena asinthe dzina lake ndipo linabwelera kukhala Zaid bun Haarithah. Aayah yake ndi iyi: Ayitaneni ndi maina a atate awo. Kutero ndi chilungamo kwa Allah. Koma ngati simukuwadziwa atate awo, aitaneni ngati abale anu pachipembezo, komanso ndi anzanu... Ahzab:5 Mtumiki (saw) ananena mu Hadith kuti Yemwe angadzitchulire dzina loti si la bambo ake, kumachita akudziwa kuti iwo si bambo ake, ndithu Jannah ndi haraam kwa iye.Kutanthauza kuti kutero ndi haraam/zoletsedwa. Mutawauza bambo anuwo kuti mukutenga dzina la bambo anu enieni, ndikukhulupilira kuti in shaa Allah adzakumvesetsani inu ngati mutakambirana nao mwanzeru, poti iwo akuzindikira mbiri yanu yonse. Komanso osalephera kuwalongosolera Aayah ndi Hadith zimenezi kuti akhulupilire kuti inu simungokamba za mmutu mwanu. Allah akutsogolereni ndikukhazikitsa mtendere ndi chikondi pakati pa inu, bambo anu komanso banja lonse. Zikomo malawiummah/article/61346/kusintha-dzina-la-bambo-omubereka-ndikutenga-la-bambo-omupeza.html --------- Ngati muli ndi maganizo ena pa funsoli, ndemanga kapena kutiwongolera malinga ndi mmene tayankhira, lembani mmusimu.
Posted on: Sat, 11 Oct 2014 19:48:35 +0000

Trending Topics



ass="stbody" style="min-height:30px;">
https://youtube/watch?v=ii3H0-zaTyY&hd=1 Karim Shah Mohamed Omar
So we take the decision to do nothing it has it pros and drawbacks
COUNTRY FOCUS : COTE DIVOIRE ( IVORY COAST). DEMONSTRATION OF
OPIS METODY NAUCZANIA PRZEWAGA METODY CALLANA NAD METODĄ
Women across the globe bring innovation to the world’s

Recently Viewed Topics




© 2015