Ife a MW EFF sitizalora sankho chifukwa cha kusiyana kwa khungu - TopicsExpress



          

Ife a MW EFF sitizalora sankho chifukwa cha kusiyana kwa khungu lamunthu, timakonda wina aliyese. Komanso sitizalora kuti munthu oyela, mzungu, mwenye, kuti aike zofuna za anthu ake patsogolo kusiya anthu a dziko la Malawi. Ife a MW EFF tizaika zofuna za munthu wa dziko lino munthu wakuda, mzungu kapenaso mwenye amene ali nzika patsogolo. Ndizomvesa chisoni kuti pamene matenda a Ebola afika povuta ndipo anthu akuda ambiri amwalira, zadziwika kuti boma la America likusunga mankhwala amene lapasa ma dokototala awiri amene anagwidwa ndi matemdawa. Izi ndizokhumudwisa ndi kumvesa chisoni kuti moyo wa munthu wa Africa ukutengedwa ngati nyerere lero ilipo mawa yapondedwa. Chonde tikufuna munthu wakuda adziwe agenda ya mzungu ndi yosamala mtundu wake, ifeso tikufuna agenda yathu ikhale yosamala anthu anthu. Zikomo
Posted on: Tue, 05 Aug 2014 10:41:42 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015