JOSEPHY NKASA WAKWIYA TSOPANO Lyrics :Josefe Mkasa VERSE Chomwe - TopicsExpress



          

JOSEPHY NKASA WAKWIYA TSOPANO Lyrics :Josefe Mkasa VERSE Chomwe munthu wamkulu akuchiona atakhala pansi Mwana sangachione olo ataimilira Economic recovery plan Malawi yativuta Taonani yayamba kutulutsa minga Mfumu inatiuza kuti potha miyezi 18 Chuma cha dziko la Malawi chiyamba kuyendanso bwino Lero tiku’uzidwa kuti Kwacha yalimba tsopano Iri ndi mphamvu, mukunamiza mafuko Ngati Kwacha iri ndi mphamvu bwanji mitengo ya katundu Ikukwerabe, sikutsika mitengo Mafuta agalimoto akumatsika mtengo Kutsitsa akunenako atsitsa ndi K10 CHORUS KULIRA KWA AMPHAWI KWAMVEKA DZIKO LONSE KULIBE AKUTIMVA AYANG’ANA KUMBALI ONSE PAGULU LAWO AONJEZA MAKANI ATI TIZITAKATA IFE TITAKATA BWANJI? POMWE TIRIBE MPAMBA ZOMWE TIKADALIRA KALE ZIDALEKA KUYENDA VERSE Mayiko anzathu tidayandikana nawo Ndi otukuka, anthu ambiri alemera Mavoti awo adasankha amuna ochita malonda, otha bizinesi Chitsanzo ku Mozambique anthu adavotera ndani? Armando Guebuza munthu wa bizinesi Pa Zambia pomwepa wanthu adavotera ndani? Micheal Sata munthu wa bizinesi Pitani ku mayiko awo mukapeze n’kotukuka Sungayerekeze n’pano pa Nyasaland Nafenso a Malawi tichite chimodzimodzi Tisankhe munthu ochita bizinesi CHORUS KULIRA KWA AMPHAWI KWAMVEKA DZIKO LONSE KULIBE AKUTIMVA AYANG’ANA KUMBALI ONSE PAGULU LAWO AONJEZA MAKANI ATI TIZITAKATA IFE TITAKATA BWANJI? POMWE TIRIBE MPAMBA ZOMWE TIKADALIRA KALE ZIDALEKA KUYENDA Nkasa sadzatheka ayi
Posted on: Wed, 18 Sep 2013 06:53:51 +0000

Trending Topics



eight:30px;">
Market Update : Cost of borrowing falls for real estate
Cyber Monday and Black Friday Sony 128 MB MagicGate Memory Stick
Ok, AVOID THE MOTOROLA DROID4 LIKE THE PLAGUE. I got one less than
CERAH, CANTIK & GEBU DENGAN AURAWHITE CHOCOLATE INDULGENCE: -
CREMA LIPOREDUCTORA : ESTA FORMULADA EN BASE A PELO , SU FORMULA

Recently Viewed Topics




© 2015