Macheza pakati pa HIV ndi Ebola! HIV: Wawa madala! Ebola: Yes - TopicsExpress



          

Macheza pakati pa HIV ndi Ebola! HIV: Wawa madala! Ebola: Yes achikulile HIV: hahahaha! Achikulile ndinu ine anthu akungondiseka akuti ndatha sakundiopanso ati ndinali kale.. Ebola: kkkkkkkkk akutelo eeeti? HIV: eeetu amwene oti masiku ano anthu sakundikamba-kamba ati andipandila zida zambili monga: Chishango,Manyuchi ndima ARV, oti pano amwene aaaah ndatha basi koma nkhani ili mkamwa- kamwa ndiyaiwe dziko lonse likukuopa ati wabwela ndi muraro ndipo sukunyengelera ukusesa heavy tandiuze chinsinsi chako mzanga?? Ebola: Aaaaah zazingono amwene chimafunika ndichangu pamalo komanso osanyengelela inu mumachulutsa chisoni amwene mumudwalitse munthu kwanthawi yaitali mpaka awonde mkumamutenga bwino ife tikumangobwela ndiya ululu amwene 3weeks ndamtenga! HIV: ndiye ku malawi kuno mubwela liti chifukwa fans ndiye ili nje-nje-nje! Ebola: Aaaaaah ndiganize kaye bwino chifukwa ndamva kuti a malawi anditchelela makhwekhwe mma border onse kuti ndikamalowa ndikodwe ndipo andiphe ndiye ndikufuna ndiyilingalire kaye kuti ndidzalowe mwa style amwene! HIV: bwelani amwene tidzathandizane chifukwa ine ndee sindikulimbatu amwene! Ebola: osadanda mzanga ndidzakupeza pano ndikuzula ma pwepwete kaye! HIV: okay mudzatipeza! Ebola: okay bye! HIV: bye! #Smigle_BM3
Posted on: Sat, 09 Aug 2014 13:22:45 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015