Mbava zoba ndi mfuti zinalowa banki lina modzidzimutsa. Wamkulu - TopicsExpress



          

Mbava zoba ndi mfuti zinalowa banki lina modzidzimutsa. Wamkulu wa mbavazi anati Aliyense agone pansi, ife tikungofunako ndalama osati moyo wa wina.... ………… Uwu timati mutu wa nkhani_munthu ukamakamba chinthu chizikhala ndi mutu kuti anthu azidziwa chikuchitika.. Mbava zitalamula anthu onse anagona pansi, Mai wina anagona mwadama koma wamkulu wa mbavazi anati, Mai gonani bwino_bwino chifukwa ife si ogwilira ayi ……… Uku timati kulondoloza ntchito. Munthu ukafika pamalo ndi bwino kumapanga icho wabwelera... Mbavazi zitaba ndalama, mbava ina inati tiyeni tiwelenge kuti taba ndalama zingati.. koma mkulu wambavazi anati... kuti tiwelengere mommuno atigwira, tiyeni tithawe timva pa TV alengeza machulukidwe andalama zomwe taba... !…… Uku timati kudziwa bwino ntchito( experience) kukhala ndi experience ndi chinthu cha mtengo wapatali kuposanso mapepala……… Mbava zitapita mkulu wa banki anawuza wachiwiri wake omuthandizira kuti ayimbe foni kupolisi mwachangu koma wachiwiri kwa wa mkuluyi anati, bwana bwanji kandalama tinasokoneza kaja tingokankhiranso pomwepa? mogwilizana onse analulutira navomelezana namati chikhala mbava zimabwerabwera bwezi zikoma.... ……… Uku timati kupha nkhawa..._izikhalapo nthawi munthu kumakondwa pamwamba pamavuto………. Posakhalitsa uthenga unaphulika pa TV.. Ndalama zokwana 1 biliyoni kwacha zabedwa pa banki lina ndi mbava za mfuti... Mbava zitawelenga ndalama zomwe zinaba zinakwana 800 sauzande kwacha... wamkulu wambava anati mayo agalu aja alemelera pa ife.... ……… Mchifukwa timati sukulu ndiyofunika, munthu ukapita kusukulu umaganiza mwachangu.…… Wamkulu wa bankili ndi wachiwiri wakeyi ananyamuka pa galimoto kwinaku akusangalara kuti zawayendera koma mosadziwika bwino galimoto lalikulu linaphonya mseu ndikugunda galimoto munali anthuwa onse ndikufera pomwepo.... ……… Nkhani ndiyakuti pamene ukuchimwa Mulungu amawona. Ukhoza kusangalara komabe dziwa kuti mphoto ya utchimo ndi imfa. Musalore kutsata njira ya oyipayo pakuti mphatso yopatsidwa ndi mwini wake Mulungu sidzetsa chisoni . . Amen. Mukhale ndi tsiku lopambana ambuye akudalitseni zikomo. #chindinho
Posted on: Tue, 16 Sep 2014 07:07:16 +0000

Trending Topics




My friend runs a local electronics recycling company and recently
This weekend my oldest and closet friend Ed Morgret and I will be
I got a good question via PM and I thought I would share here on

Recently Viewed Topics




© 2015