Mphuzitsi wa standard one anaona Austin nkhope yake ikuonesa kut - TopicsExpress



          

Mphuzitsi wa standard one anaona Austin nkhope yake ikuonesa kut wakwiya ndipo anafunsa: Austin, mvuto ndi chani? Austin: aphuzitsi, ineyo ndine wamzeru kwambiri nde ndimafuna mukandiike ku standard 5 chifukwa munomu nde ndikungochedwesa time yanga. Mphuzitsi uja poona kuti nkhani ija sakanatha kuitha ekha, anaitengela kwa a head-master ndipo anafotokoza mavuto a Austin. A head-master aja anauza mphuzitsi uja kut amupase mafunso kuti aone ngat Austin akuyenela kukhaladi mu standard 5. Mphuzitsi uja anaitana Austin ndipo mafunso anayambika: Mphuzitsi: Austin, 12x12-12 ndi chani? Austin; 132. Mphuzitsi: 15-12x5x5 ndi chan? Austin: 75. Mphuzitsi uja anafunsa zambiri mpaka anapitanso kwa ahead-master aja ndipo anat Austin ofunikadi akhale mu standard 5,,,,akuyankha zolondolo zokhazokha. Ahead aja anati; mubwelesen kuno nanenso ndimufunseko zanga. Austin atalowa mu office mwa a head zinali chonchi: Ahead; Austin; ndi chani chimene ngombe ili nazo 4 koma ine ndili nazo ziwiri? Austin: miyendo. Ahead: ndi chani chimene ine ndili nazo mu mkabudula mwanga ndipo iwe ulibe? Mphuzitsi uja amavela zimenezo amaganiza kut yankho la funso limene lija ndi tsitsi koma Austin anayankha: matumba. Ahead: ndi malo ati amene azimayi amakhala ndi tsitsi lopotokolana? Austin: mu Africa. Ahead; ndi chani chimene chimalowa chouma koma chimatuluka chitafota? Austin: spaghetti mu poto. Ahead: ndi chan chimene chimayamba ndi B ili ndi C pakati ndipo kuti ugwilise ntchito zimafunika kutsekula miyendo? Austin: bicycle. Ahead: ndi chani chimene chimene chili ndi bowo pakati ndipo umafunika kuwenga ma kadabo kuopa kukala kut ulowese chala pa bowopo? Austin: CD. A head: ndi chani chimen ndi chofila mutu ndipo azimayi amasiku ano amaigwila ndikuika pakamwa? Austin; lipstick. Ahead aja anatembenuka kumene kunali aphuzitsi aja ndipo anati; mwanayi asakhalenso mu standard 5.... kuyambila lero ndi DEPUTE wanga. Mphuzitsi uja anati: simukunama...chifukwa ine mafunso amenewo mayankho ake anali otukwana okha-okha. #kabotolo#
Posted on: Sat, 08 Nov 2014 12:20:09 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015