NAWU UTHENGA WA MARIATONA!! MU OCTOBER 2014 Uthenga kwa onse - TopicsExpress



          

NAWU UTHENGA WA MARIATONA!! MU OCTOBER 2014 Uthenga kwa onse okonda kumvera Radio Maria Malawi! Akuluakulu oyendetsa ntchito za Radio Maria Malawi akudziwitsa Abwenzi a Radio Maria ndi omvera onse kuti kuli ulendo wa masiku atatu wothamanga ndi Amai Maria ncholinga chofuna kusakasaka chithandizo chothandizira Radio Maria Malawi. Ameneyu ndi Local Mariatona , kapena kuti Mariatona wathuwathu kuno ku Malawi ndipo alipo kuyambira pa 3 mpaka pa 5 October 2014. M’masiku atatuwa, Radio Maria idzakhala ikuwulutsa ma pologalamu apadera omwe cholinga chake ndikupeleka mwayi kwa inu omvera athu kuti mudzathe kuthandiza ndikupeleka lonjezo la ndalama kapena katundu wina yemwe mungakhale naye , pothandiza wailesiyi ndi kuti ithe kukwanitsa kupeza ndalama zokagwilitsira ntchito zomangira ma Transmitter atsopano m’madera awa: Thyolo, Mzuzu, ku Karonga ndinso ku Dwangwa kuti Uthenga wa Ambuye ufalikire ponseponse m’dziko lathu lino la Malawi. Abwenzi a wailesiyi akunja kwa dziko lino ku maiko ena atithandiza kale mwaulele ma transmitter omwe tikuyenera kuyika m’madela atchulidwawa . Ife ntchito yathu ndi yogula ndi kumanga zipilala zopachikapo ma antenna , komanso kumanga nyumba yosungiramo zida za transmitter. Transmitter imodzi idzadya ndalama zosachepera 25 million kwacha. Komabe paja amati pangono pasiyana mchabe tiyeni tonse tichitepo kanthu popereka kangachepe kothandizira ntchito-yi ndikuti amzathu mmaderawa azilandilanso uthenga wachipulumutso monga ife timachitira kudzera pa Radio Maria. Mungathe kupereka chithandizo chanu kudzera m’njira izi: Ku Bank; imodzi mwa ma Account awa: Account Name: Radio Maria National Bank of Malawi Standard Bank NBS Bank Mangochi Service Centre Mangochi Branch Mangochi Branch 399892 0140077298700 0045652268017 First Merchant Bank Malawi Savings Bank FDH Bank Mangochi Branch Mangochi Branch Mangochi Branch 0291194449 1022787591001 6500000027078 INDE Bank Opportunity Bank Mangochi Branch Mangochi Branch 0150676610116 1026809607618 Mukhoza kupereka chithandizo chanu potumiza maunitsi kudzera mu njira ija ya Me2U pa nambala izi: 0999-805-056, Kapena 0884-594-554 Kapena kutumiza ndalama zanu kudzera mu njira ya airtel money pa 0996-104-717 kapena TNM Mpamba pa 0882-550-950. Mukhoza kuperekanso chithandizo chanu kapena kudziwa zambiri kudzera ku ma studio athu awa: Mangochi Main Studio polankhula ndi a Promotion Manager pa 0999-560-464 Zomba Sub Studio kwa studio clerk pa 0995-243-867 Limbe Sub Studio kwa Studio Clerk pa 0995-261-102 Dedza Sub Studio kwa studio clerk pa 0999-464-604 Lilongwe Sub Studio kwa studio clerk pa 0884-676-663 Mzuzu Studio kwa studio clerk pa 0888-534-115 Ngati mufuna kupereka lonjezo-pledge-tumizani lonjezo lanulo pa manambala awa: 0888-387-995 ndi 0996-962-895 kapena kuyimba pa nambala izi> 01599 627 kapena 0993-573-579. Tiyeni tithandize wayilesi ya Maria Woyera kuti ikwanitse kufalitsa uthenga wa chipulumutso kwa anthu onse. Kumbukirani kuti tikumvera Radio Maria lero chifukwa ena anachitapo kathu pothandiza wailesi-yi.
Posted on: Fri, 12 Sep 2014 17:40:19 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015