NDIINE OKOMZEKA KUTULA PANSI UDINDO- MSUNGAMA. Chairman wa team ya Big Bullets wati iwo sakachitila mwina koma kutula pansi udindo wawo lelo ku shire highlands komwe kukakhale mkumano wa timuyi ngati iwo akapezeke kuti ndiye akusokoneza ndalama za timuyi. Pakhala pali kusamvana pakati pa Msungama komanso ochemelela ena pomwe Msungama amadzuzdzula ena mwa ochemelelawa kuti anatenga ndalama za timuyi pakati pa masewelo a Bullets komanso Red Lions ndipo pofuna kuthetsa izi timuyi lelo ikuenela kukumana kuti athetse kusamvana komwe kulipo. #GINTY
Posted on: Fri, 05 Sep 2014 06:14:06 +0000