Nkhani Zomwe zalembedwa mu news paper komanso kuwulutsidwa pa - TopicsExpress



          

Nkhani Zomwe zalembedwa mu news paper komanso kuwulutsidwa pa mawailesi osiyanasiyana m’dziko muno Team ya Azam Tigers yati Big Buliyambe yaiwala malingaliro ake ofuna kugula katswiri wa team’yi Isaac Kaliyati kamba kakuti osewerayu Sali ololedwa kuchoka ndipo kuti Tigers imudalira kwambiri pa malingaliro ake ofuna kutenga TNM Super League mu 2015. Yemwe wanena izi ndi team manager Steve Madeira pomwe watsindika kuti Big Bullets sigula katswiriyu. Bullets ikufuna Kaliyati kuti akalowe m’malo mwa Fischer Kondowe yemwe zaka zake zoswera mpira zikupita ku mapeto……….. Nkhaniyi inaulutsidwa pa MBC Radio 1. Company ya Senjere yathetsa milandu yake yomwe idasumira Mighty Wanderers komanso Super League of Malawi (SULOM) kamba kophwanya pangano pa za ma uniform omwe Company’yi imapereka ku team’yi. Bwalo la milandu ku Lilongwe lidalamura Mighty Wanderers kupereka $10 million yomwe ndi pafupifupi K4.7 billion ku Nsenjere pomwe team;yi idapezeka yolakwa pa nkhaniyi. Koma Nsenjere yati yathetsa nkhaniy ndipo m’malo mwake ikambilana ndi mbali ziwirizi kunja kwa khoti komanso iwunikire bwino za mgwirizano kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino. Pakadali pano, team ya Big Bullets yati nayonso ikhala pansi ndi Senjere kuti ikambilane ngati nkotheka kuyamba kugwiritsa ntchito ma uniform a company’yi…….. Nkhaniyi yaulutsidwa pa Zodiak Team ya Airborne Rangers yati chaka cha 2014 chidali chopambana ku team’yi kamba kakuti ndi team yokhayo yomwe idalowa kumene mu TNM Super League koma sidatuluke. M’modzi mwa akuluakulu a team’yi ndi yemwe wanena izi ndipo wati chaka cha mawa, Airborne Rangers idzapanga zotheka kuti idzamalize mu ma team ochita bwino ndi cholinga chodzasewera nawo Standard Bank…………. Nkhaniyi yaulutsidwa pa MBC Radio 1. Mlembi wa team ya Big Bullets Harold Fote wati team’yi ikukonza masewera ongopimana mphavu ndi team ya Mamelodi Sundowns ngati njira imodzi yokonzekera mpikisano wa CAF Champions League chaka cha mawa. Fote wati zonse zikuyenda bwino ndipo kuti zikatheka, adziwitsa mtundu wa a Malawi. Fote amapitilizanso ponena kuti pa 31 December, otsatira a team’yi adzakhale akuwuzidwa za osewera oatsopano omwe adzaitumikire team’yi mu CAF kamba kakuti zokambilana ndi ma team omwe osewerawa amasewera zili mkati ndipo zikuyenda bwino. Fote sadatchule osewerawa koma MSLNSF ili ndi umboni onse kuti Richard Chipuwa ndi Francis Mulimbika a Mighty Wanderers, Isaac Kaliyati a Azam Tigers, Shumaker Kuwali ndi Junior Malidadi a Blue Eagles komanso Lucky Mlata ndi Chawanangwa Kaonga a Silver Strikers ndi omwe akukambilana nawo. Fote adatsina khutu tsamba lino kuti zonse zikuwayendera ndipo ali ndi chikhulupiliro kuti zonse ziyenda bwino. Team ya Silver Strikers yati Frank Banda ndi Chawanangwa Kaonga akachoka ku team’yi, padzapezeka ena omwe adzathandize m’malo mwa anyamatawa. M’phuzitsi wa team’yi Stain Chirwa ndi yemwe wanena izi ndipo wati ngati anyamatawa achoke, iye angowafunira zabwino zonse kamba kakuti zimafunika osewra kumayenda ndikumaona zinthu zina zosiyana. Pali mphekesera kuti Frank Banda wake wapsa wa ku Mozambique pomwe Kaonga atha kupita ku South Africa kapena ku Big Bullets… Nkhaniyi yalengezedwa pa MBC Radio 1 Izi ndi nkhani zina zomwe zamveka tsiku la lero. M’malo mwa ma admin anzanga, MSLNSF ikukufunilani Znyengo yapamwamba ya Christmas komanso chaka chatsopano chopambana, zikomo kwambiri chifukwa chokhalabe ndi tsamba lino, mumakwanaa……………@Andy
Posted on: Thu, 25 Dec 2014 06:03:28 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015