Nkhani ya chisoni. GERALD NGALAUNDE WAZIMPHA. Gelard Ngalaunde - TopicsExpress



          

Nkhani ya chisoni. GERALD NGALAUNDE WAZIMPHA. Gelard Ngalaunde yemwe amadziwika kwambili ndi dzina loti Lampardochokera ku Ekwendeni {Mzimba} wanfa infa yowawa kwambili atazimangilira ndi chingwe ku Parow dzulo Mmawa kusiya nkazi wake Doreen atangofika kumene. NKHANI: Gelard anaudza makolo ake kuti ampedzere nkazi kumudzi,makolo ake adachitadi zomwe iye akafuna ndipo adapedzera chimphadzuwa chamudzi mwake momo Doreen,awiliwa adali ataonanapo kale kumudzi koma sanakhalepo pa chibwezi kapena kugonana,Gerald adapangitsira nkazi wake chilichotse kuphatikiza passport ndi transport yochokera ku Ekwendeni mpaka CapeTown poti Makolo a Gelard komatso Doreen ndi anthu opephera kwambili kumudzi iwo sadafune ana awo kulowa Banja kopanda kumangitsa chikwati. Doreen atafika,iye adalandilidwa ndi achibale a Gelard mayi Frola omwe amakhala ku Constacia,apa kuti Gerald atakhozekera kale zaukwati,patadutsa matsiku angapo,awiliwa ndi bambo Lameck adapita kukayedzetsa maganzi,thawi itakwana youlutsa zosatira ndi pamene dokitala sadabisile kuti Gerald ali ndi kachilombo koyambitsa Matenda a AIDS,akuti apa Gerald analira komatso kupanga manyazi kwambili.Atafika kumudzi achibale anakambilana ndipo iwo adati banja silingakhalepo koma Doreen abwezera ndalama nzake Gelard akayamba tchito.Akuti Gerald analibe nazo tchito koma azanke komatso wina aliyetse adadziwa kuti iye ali ndi AIDS,malingana ndi otitumizira nkhani komatso zomwe yalemba newspaper ya The daily Sun pa tsamba lake lachitatu,akuti Gelard amapanga manyazi yekha kumayenda komatso kumapita ku church poti wina aliyetse anadziwa zankhaniyi.Amalawi akuti Gerald anapasidwa matenda ndi Mtsikana wina wachitonga emelida ochokera ku kavuzi [Nkhata-bay]Yomwe amagonana naye.Kufikira dzulo Mmawa,Gelard anaganidza zochotsa moyo wake ndi kusazikana ndi dziko.Akuchimuna akwiyira akuchikazi kuti ndiwo amafalitsa ku Anthu zoti Gelard ali ndi AIDS.Gelard wamwalira ali ndi nzaka 26.Dongosolo lotse la ifayi tikhala tikulengezabe. #Mzimu ya zochitika ndi yokhumudwa kwambili ndi ifayi. No fear No favour. Zochitika pa CapeTown
Posted on: Fri, 10 Oct 2014 06:54:37 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015