Nthabwalist ankathamangitsa kwambiri Galimoto, tsiku lina wa speed - TopicsExpress



          

Nthabwalist ankathamangitsa kwambiri Galimoto, tsiku lina wa speed trap anamugwira zinali chonchi: Traffic policeman: Takuimitsani chifukwa chothamangitsa kwambiri galimoto, ndione nao Licence yanu? Nthabwalist: Licence ndilibe inanditaika ku mowa. Traffic policeman: Aaaaa chabwino give me registration papers? Nthabwalist: Ndilibenso mapepala mukunenao chifukwa galimotoyi ndinachita kuba mwini wakeyo ndinamupha ndinamutsekera ku boot inu simukumva kununkha? Wa police uja atangomva izi anadziwa kuti waimitsa chigawenga nthawi yomweyo anaimbira phone anzake kuti abwere, sipanathe 10 mins siren inamveka apolice ambiri anafika ndi mfuti zao mmanja Wa police mmodzi anamuloza Nthabwalist ndi mfuti kumuuza atsike mugalimoto Nthabwalist anatsika “Licence ili kuti?” anafunsidwa Nthabwalist....Nthabwalist anatenga Licence ndikupereka kenaka anamuuza atsegure ku boot....Nthabwalist anatsegura koma kunalibe chilichonse...Wa police uja anadabwa mpaka anafunsa “kodi mesa tamva zoti mulibe Licence komanso kuti munapha munthu ali ku boot?” Nthabwalist anayankha nati “ iiiiiiiiii amakunamizani ndiwabodza kwambiri ameneyu mwinanso akunamizani kuti ndimathamingitsa galimoto” pepani amwene takuchedwetsani mutha kumapita awa tikathana nao ku ntchito....Nthabwalist kuliza machine wautali....
Posted on: Wed, 17 Dec 2014 17:05:34 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015