Nyamata wina yemwe anapita ku Theba kukagwira ntchito zamuvutako - TopicsExpress



          

Nyamata wina yemwe anapita ku Theba kukagwira ntchito zamuvutako chifukwa chosawupeza ntima,Ma report akuti nyamatayu amachokera mboma la Mangochi ndipo iyeyu atafika ku Theba sanaupeze ntima atawona ana azimai oyera ngat angelo omwe kuno kwathu sangafikire oro atakhala ndi ma million.Nyamatayu yemwe ndi okwatira komanso ali ndi atatu kumudzi kuno wakhala akusinthasintha azimai ku Thebako .Koma amati la chi fote imakwana anapezana ndi calad wina yemwe amaoneka ngati ndionenepa koma osadziwa kuti inari mimba ya mamuna wina.Adawa anazuzulidwa komano calad naye anamukanitsitsa kuti ayi ndithu ndikukhala kwake.Pangotha miyezi inayi yokha kapena kuti 4 nkaziyu wachira lero ali ndi mwana wa nkazi .Anthu ozungulira derari amuseka nyamatayu kamba kosalabadira moyo wake komanso umphawi wake omwe anausiya kuno kumudzi .Tikunena pano anthuwa akukhalabe limodzi pamene nkaziyu wakakamira nyumbamo kuti ngat atamuthamangitsa ndiye kuti mamunayo zake zida amukwezetsa ndege yopanda mipando ija.Chenjezo kwa anyamata ndi asungwana omwe mumakhala kunja kwa dziko lathu lino kuti samalani muliko chifukwa kwanu kwanu nthengo mudalaka njoka ndipo ngati simusintha ndiye kuti muzabwera muli chibadwireni kapena mulibe kalikonse. Malangizo ndi awuere
Posted on: Wed, 10 Jul 2013 21:45:48 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015