A Peter Mutharika akulingalila zosaima nawo pachisankho cha chaka - TopicsExpress



          

A Peter Mutharika akulingalila zosaima nawo pachisankho cha chaka cha mawa chifukwa cha milandu Nkhani yongotipeza kumene ndiyakuti mtsogoleri wa chipani ca DPP a Peter Mutharika auza anthu omwe amawakhulupilira kuti akuganiza zosaima nawo pa masankho a chaka cha mawa chifukwa cha zomwe boma lachita kuyamba kufufuza chuma ndi katundu wa boma zomwe zakhala zikubedwa kuyambila pa nthawi yomwe mkulu wao malemu Bingu wa Mutharika anayamba kulamulira dziko lino. A Peter Mutharika akuganizilidwa kuti anali nawo mgulu losakaza chuma cha boma ndipo eni ake akuziwa kuti ndi umboni omwe ulipo ndizoputa kupulumuka mu chipululu chimenechi. Tikhala tikukupasilani nkhani yonse mwasatanesatane chaku masana kuno.
Posted on: Sat, 26 Oct 2013 05:39:11 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015