Anati ndizakhala mwezi umodzi ndi - TopicsExpress



          

Anati ndizakhala mwezi umodzi ndi ndani?...Ramadhan #Namzy Mmodzi mwa aphunzitsi a timu ya Big bullets Nsazwirwimo Ramadhan yemwe kwawo ku Burundi ndipo anabwera kuzathandidza timuyi kuti itenge ligi watsusa zomwe zinamveka kuti adzakhala mdziko muno mwezi umodzi. Nkhani yokhala mdziko muno ndi yapakati pa ine ndi a immigration nde ndikudabwa kuti anthu ankazitenga kuti zoti ndikhala ku Malawi kuno mwezi umodzi,ine ndidakali konkuno mpaka mmene nditafunile,anatero Ramadhan loweruka pa kamuzu stadium timu yake itakwapula timu ya Karonga utd 3-1. Izi zikusiyana ndi zomwe adanena akulu akulu a timuyi kuti Ramadhan akubwera ku Malawi pa tchuti ya mwezi umodzi ndipo kuti timuyi idzampasa 1 million kwacha pogwira ntchito ndi timuyi.Ramadhan anabwera mdziko muno pa 01 October chaka chino ndipo amayenera kubwelera ku South Africa pa 01 mwezi uno kutengera zomwe adanena akulu akulu a Bullets.
Posted on: Mon, 03 Nov 2014 06:45:59 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015