UTHENGA WANTHU WALERO!!! Bambo analowa mnyumba kuwuza mkazi - TopicsExpress



          

UTHENGA WANTHU WALERO!!! Bambo analowa mnyumba kuwuza mkazi wake. Bwera panja udzawone galimoto lomwe ndagula... Linali galimoto la pamwamba la BMW. Banjali lomwenso linali ndi mwana mmodzi wachichepere, linanyadira kwambiri ndi galimotoli. Tsiku lina bamboyi akutsuka galimotoli anawona mwana wakeyi akulemba mzera ndi msumali omwe unali mmanja mwake. Mokwiya bamboyi anatenga chimtengo namenya mwamphamvu dzanja la mwanayi ndikumuvulaza kwambiri zala. Atafika naye kuchipatala ma dotolo sanachitire mwina koma kuduliratu zala za mwanayi. Patatha masiku angapo mwanayi ali chigonekere kuchipatala, anapenyetsetsa bambo ake nafusa, KODI ADADI, ZALA ZANGA ZIMELA LITI? Bambo anagwidwa ndi chisoni kusowa choti mkuyankha, anangochoka ndikumakalira kuseri pozindikira kuti mzera unali pagalimotoli mkosavuta kukonzetsa koma palibe chomwe chingadzabwezel etse zala za mwana wake mpaka imfa... Kuyika mtima pazopangidwa ndi manja a munthu mkwachabechabe ndipo zimangosautsa mtima. VALUE your family than material things. Za mdziko komsavuta kupeza komaso mkosavuta kutayika, pamene mphatso zochokera kumwamba ndizapaderadera komanso zamuyaya. Family is the greatest gift of all, more worth than gold. Love your family, care for your family, bless your family ndipo ine admin ZEKO ndikuti zabwino zonse zidzapatsidwa kwa iwe. Amen
Posted on: Wed, 16 Jul 2014 19:06:42 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015