Boma la Malawi kudzera mu Unduna wa zamalimidwe wayamba ndondomeko - TopicsExpress



          

Boma la Malawi kudzera mu Unduna wa zamalimidwe wayamba ndondomeko yolembera makoponi ija imatchuka kuti SUBSIDY mdziko lonse la Malawi sabata ino. Tati tikudziwitseni kuti ndondomeko ija imanena a DPP ya makompyuta sitheka madera onse MMalawi muno kamba ka zovuta zina. Kotero angosankhapo maboma angapo kuti akhale oyeserera ndondomeko ya makompyutai. Pali maboma angapo amene asankhidwa kuti aeserere njira ya Biometric system(E-voucher) monga ngati boma la Nsanje, ndondomekoyi aeserera kwa T/A Tengani kokha. Komanso poonjezera apo ndondomeko ya makompyutai igwila ntchito pogula mbewu zokha osati feteleza.
Posted on: Tue, 05 Aug 2014 03:49:19 +0000

Trending Topics




© 2015