MULUNGU NDI WABWINO NAWU UMBONI true story Wokondedwa ndati - TopicsExpress



          

MULUNGU NDI WABWINO NAWU UMBONI true story Wokondedwa ndati ndichitire umboni pa za ukulu wa Ambuye.Ndine #Maureen_Banda dzulo usiku nditagona ndimalota ndikumvera nyimbo zauzimu zomwe zinayimbidwa ndi #Thoko_Katimba. Kumalotoko ndidali wa chimwemwe ndithu sindimadziwa kuti kunja kulinji.Abale pa nthawiyi nkuti anthu akuba ali ku mpanda kwathu. Kutulo komweko ndinatuluka anthu akuba aja anandifusa akuti abwana ako ali kuti?..Sindinayankhe amafuna andiombere ndi mfuti koma mzungu wanga anakuwa ndipo amalira nati,Maureen leave them alone!.Let them have what they want in the property pliz!.I dont want to loose u pliz Maureen!.. Kenaka ndinadzidzimuka chifukwa ndimafuwula kuti,Jesus!.. Ndinagona ndi ma headset nditachotsa ndinamva agalu akuwuwa nditatuluka ndinawona anthu atatu ataziphimba kumaso,nthupi langa linadzazidwa ndi mantha zedi.Ndimazilankhulira ndekha mu mtima mawu awa,Lord am not ready pliz protect me from this... Ndidangodabwa anthu aja akupita koma angokoka telera ya galimoto ya mzungu wanga ndi kumapita. Adangondisiya ine nditakhala pansi ndi mantha nditayangana nthawi nkuti ili 1am mbandakucha. Ndidaitana a security ndikumuwauza zomwe zachitika adandifunsa,eni nyumba ali kuti?,ine ndayankha kuti,ku holiday,then akuti,Ambuye alemekezeke kuti uli ndi moyo coz streat yomweyo plot ina mzungu ndi agalu ake aphedwa ndi akuba. Misozi inatsika mmasaya angamu ndi chisoni. Abale ndi alongo tiyeni tizimuyamika Ambuye nthawi ina iliyonse. Atate athu akumwamba ndikudziwa ndizambiri zochitika mkati mwausiku mutetezeni ndi kumuyanganira mbale ndi mlongo mkati mwa usikuwu.Mu dzina la Yesu Khristu AMEN.. #advisor02
Posted on: Wed, 30 Jul 2014 18:15:21 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015