Piyasi ndi Austin anapita ku interview ya - TopicsExpress



          

Piyasi ndi Austin anapita ku interview ya ntchito...anayamba kulowa mu office ndi Piyasi. BWANA anayamba kufunsa: President oyamba waku Malawi anali ndani? PIYASI: Kamuzu Banda. BWANA: anabadwa liti? PIYASI: 1898. BWANA: ndizoona zoti mankhwala a Edzi anapezeka? PIYASI: eya koma sizinatsimikizidwe ndi boma. BWANA anati: iwe wayankha bwino kwambiri,,pita ukadikilire ma results ako panja,,umuuza ali panjayo alowe. Piyasi atatuluka anakumana ndi Austin panja ndipo anati: pita ukalowe mu office mo ndi nthawi yako.. AUSTIN anati: koma sakufunsa zolimba bwanayo? Tangondiuza ma answer kuti ndikakhozenso nane. PIYASI anati: 1: yankho lake ndi Kamuzu Banda. 2: yankho lake ndi 1898 ndipo 3: ndi eya koma sizinatsimikizidwe ndi boma kenako Austin analowa. BWANA: dzina lako ndani? AUSTIN: Kamuzu Banda. BWANA anazunguzika mutu koma anafunsanso: unabadwa liti? AUSTIN: 1898. BWANA anakwiya ndipo anati: kodi ndiwe wamisala eti? AUSTIN anayankha: eyaa koma sizinatsimikizidwe ndi boma. Bwana anakomoka.
Posted on: Fri, 30 Aug 2013 19:09:33 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015