Dzulo nditamva kuti anzathu adera lina lake akhunzidwa kwambiri - TopicsExpress



          

Dzulo nditamva kuti anzathu adera lina lake akhunzidwa kwambiri ndi ma floods moti ena atisiya, koma otsalawo akukana kupulumutsidwa ngakhale boma la Malawi lakonza njira zowapulumutsira; talk of helicopters, rescuing boats etc, ineyo sindinangomva chisoni chokha ayi koma ndinawafanizira anthuwo ndi zomwe ifeyo achinyamata timachita. Anthu ambiri akulu akulu plus achinyamata ambiri we blamed anthuwo kuti akuononga ndalama za boma, ena ananena zambiri ndithu. Anthuwadi seriously sanachite bwino koma I have some questions for you wisest ones; 1. Kodi ndiangati mwaife amene sitiliilitsa makolo athu ndizochita zathu? Makolo amaononga ndalama zambiri, ndalama zoti banja lonse linakapindula nazo zimathera paife koma mpamene timapita kukashosha mimba yosakonzekera makolo nkumalira. Makolo qmafika pena kumapita kopemphera kuti tisiye mchitidwe oyipa, mpamene timabweretsa milandu pakhomo. Tikusiyana ndi anthu okana thandizo la boma wa? 2. Atsogoleri achipembezo chathu, ndikunena pano siafike potilirira kuti achinyamata tiziletse, tipewe kuika moyo pachiswe koma ife nkumapitilizabe kuziononga? Atsogoleri kumachititsa ma overnight, kuononga ndalama zambiri, kuti wachinyamata asinthe. Koma ayi ndithu ndalama mkumapita mmadzi. Tikusiyana bwanji ndi anthu okana thandizo la boma wo? 3. Boma komanso mabungwe omwe siaboma akuyesetsa pa nkhani yoti wachinyamata aziletse, kuyesetsatu, nkuzaona kuti sizikutheka, mimba zoyambekezera mbwee, HIV mbweee. Boma ndimabungwe nkuzati yah! Titani? nkuyamba kugawa ma condom kuti mwina, ayinso, mimba zosayembekezera mbwe pakati pa achinyamata, HIV new infections nkumachulukabe pakati pa ife achinyamata, kodi tikusiyana pati ndiokana kukwera ndege aja omwe akutenga thandizo la boma for granted? 4.Ma program okhunza kupewa HIV and other STIs plus unplanned pregnancies, olimbikitsa maphunziro etc ali mbwee pa TV, Radio komanso mmabungwe otsogoleredwa ndi achinyamata, koma wachinyamata nkumatengabe HIV, STIs and unplanned pregnancies. Kodi do we know how much a 30 minute radio and TV program costs? Guys ndizodula kooooopysa. Nde wachinyamata nkumakanikabe even after ulangizi onseu kodi sichimodzimodzi anthu akukakamira mmadziwo guyz? 5.Pano pa fb tsiku ndi tsiku tikumalangizana mmene tingakhalire athanzi. Kupezeka pa fb guys sikotchipa. Its very expensive koma timakhalabe mpaka madzulo. Ndalama zathu zomwe nkumapita koma ife osasinthabe, kodi tasiyana bwanji ndi anzathu okakamira malo amakolo awo ngakhale ali pachiopsyezo? Wiseat ones, receive my warmest greetings.
Posted on: Fri, 16 Jan 2015 05:20:12 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015