CHOFUNIKIRA PAKATI PA NDALAMA ZA NAC NDI KUSOWA KWA JB PA MALAWI - TopicsExpress



          

CHOFUNIKIRA PAKATI PA NDALAMA ZA NAC NDI KUSOWA KWA JB PA MALAWI Zaka 50 a Malawi tikadakasekelerabe anthu omwe akhala akuba chuma mboma nkumatigaila. Koma kuwaukira Iwo omwe akulimbana ndi mbavazi... Mabungwe omwe si aboma ndi atsogoleri awo monga Gift Trapes, Martha Kwataine ngakhalenso andale monga Jessy Kabwira sakudziwabe kuti pomwe pali anthu awiri pakusoweka kukambirana nkhani za HIV, AIDS ndipo ngati pena pake pali thandidzo la ndalama zikuyenera kuwafikira anthu oterewo ngati kuthekera kutakhalapo. Nkhani ya ndalama zomwe zikusowetsa tulo bwana Lazarus Chakwera ndi anzawo ena zochokera ku NAC kupita ku mabungwe monga Mlhakho Wa Alhomwe ndi ena. Sinkhani yoti munthu wa nzeru zake nkuitulutsila chakukhosi kapena misempha monga zikukhalira ndi a Chakwera, Martha, Jessy komanso Trapes. Aliyense akudziwa kuti bungwe la NAC zina mwa ntchito zake ndi kupereka thandidzo lina lililonse kumabungwe ngakhalenso magulu omwe cholinga chawo ndi kuthandidzira kuthetsa bvuto la mulili wa HIV, AIDS maka maka kwa Iwo omwe apempha komanso kuonetsa chidwi pa nkhaniyi. Mdziko muno tsopano tili ndi mabungwe ochuluka omwe zolinga zake ndi kulimbikitsa miyambo ndi zikhalidwe za makolo potengera zikhulupilro za anthuwo ndipo kupyolera mu zikhalidwe ndi miyambo yathu komanso kamba ka umphawi ndi umbuli zaonetsa kuti matenda a HIV, AIDS akula kwambiri pakati pa a Malawi. Tili ndi mchitidwe ngakhalenso magule ena omwe timabvina munyengo zosiyana siyana kamba ka miyambo ndi zikhalidwe zathu omwenso umakoledzera kufalitsa nthenda zomwe bungwe la NAC limalimbana nawo kupyolera mzithandidzo zake. Ndiye kaya wina akufuna ndalamazo za NAC, kaya ena akuti sazibweza koma khumbo langa ndikufuna kudziwa za kusowa kwa JB pa Malawi pano atabisa report ya Cashgate kufikira kuchoka ku Sanjika.
Posted on: Tue, 16 Dec 2014 05:05:25 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015