GABADIHNO KU JONI. Lachiwelu lapitali team ya mpira wa miyendo - TopicsExpress



          

GABADIHNO KU JONI. Lachiwelu lapitali team ya mpira wa miyendo yomwe amasewera Gaba, inali ndi gonelo(dinner)yomwe inakozera mapuleya a timuyi. Chosangalatsa anasankha Gaba kuti ndiye apemphere pemphero loyamba pa dinayo. Ndipo adamuuza Gaba 5hours be4. Ndipo Gaba pozindikira kuti samatha kulankhula koma kulemba ndikuwerenga English. Analembelatu pemphero pa kapepala ndikupinda mkuika mu chisoti kumbuyo. Pomwe mwambo wa dinner umayamba Gaba sadadziwe kuti kapepa kataika . Atagwira mchisoti adaona kuti mulibe, adaganiza kuti kagwera mmalaya. Atapisa mmalaya adagwira ka lebo kaja kamapezeka mu zovala ndipo adathothola kenako amvekere : Let us pray. Pure cotton. Luke warm wash ,warm iron, do not bleach. Do not dry clean, do not tumble dry. Wash dark colours separately. Made in lesotho. Fabric made in RSA. Amen. Atatero mwambo udasokonezeka chifukwa kunali kuseka koposa uku akutinena kuti mbuli za ku malawi.
Posted on: Sun, 24 Aug 2014 21:18:35 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015